Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 24:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Amuna amene anali ndi Davidewo anayamba kumuuza kuti: “Lerotu ndi tsiku limene Yehova akukuuzani kuti, ‘Taona, ndapereka mdani wako m’manja mwako,+ ndipo umuchitire chilichonse chimene ukuona kuti n’chabwino.’”+ Choncho Davide ananyamuka ndipo mwakachetechete anadula kansalu m’munsi mwa malaya akunja odula manja a Sauli.

  • Salimo 9:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Anthu a mitundu ina agwera m’dzenje limene anakumba okha.+

      Phazi lawo lakodwa mu ukonde+ umene anatchera okha.+

  • Salimo 141:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Oipa onse adzagwera m’maukonde awo omwe,+

      Koma ine ndidzadutsa bwinobwino.

  • Miyambo 26:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Amene akukumba dzenje adzagweramo yekha,+ ndipo amene akugubuduza mwala udzabwerera kwa iye.+

  • Miyambo 28:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Munthu amene amasocheretsa anthu owongoka mtima+ kuti ayende m’njira yoipa, adzagwera m’dzenje lake lomwe.+ Koma anthu osalakwa adzapeza zabwino.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena