Salimo 7:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Iye wafukula dzenje, walikumbadi.+Koma adzagwera m’dzenje lokumba yekha.+ Miyambo 26:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Amene akukumba dzenje adzagweramo yekha,+ ndipo amene akugubuduza mwala udzabwerera kwa iye.+ Mlaliki 10:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Amene akukumba dzenje adzagweramo,+ ndipo amene akugumula mpanda wamiyala njoka idzamuluma.+ Agalatiya 6:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Musanyengedwe,+ Mulungu sapusitsika.+ Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.+