Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 34:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Kenako mudzatenga ena mwa ana awo aakazi kuti akhale akazi a ana anu aamuna,+ ndipo ana awo aakazi adzachita chiwerewere ndi milungu yawo, n’kuchititsa ana anu aamuna kuchita chiwerewere ndi milungu yawo.+

  • Levitiko 17:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Chotero asamaperekenso nsembe zawo ku ziwanda zooneka ngati mbuzi*+ zimene akuchita nazo chiwerewere.+ Limeneli likhale lamulo kwa inu mpaka kalekale, m’mibadwo yanu yonse.”’

  • Numeri 15:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 ‘Chingwecho chikhale ngati mphonje kwa inu, kuti mukachiyang’ana muzikumbukira malamulo onse+ a Yehova ndi kuwasunga. Muleke kutsatira zilakolako za mitima yanu ndi maso anu,+ chifukwa potsatira zilakolako zimenezo, mukuchita chiwerewere.+

  • Yeremiya 3:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Iye anayamba kuchita uhule chifukwa choona nkhani imeneyi mopepuka. Anali kuipitsa dzikolo+ ndi kuchita chigololo ndi miyala komanso mitengo.+

  • Ezekieli 20:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 “Tsopano uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kodi anthu inu mukudziipitsa potsatira njira za makolo anu?+ Kodi mukutsatira zinthu zawo zonyansa ndi kuchita zachiwerewere ndi mafano amenewo?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena