Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 34:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Samalani, kuopera kuti mungachite pangano ndi anthu okhala m’dzikomo, pakuti iwo adzachita chiwerewere ndi milungu yawo+ ndi kupereka nsembe kwa milungu yawo.+ Chifukwa mukachita nawo pangano, mosakayikira wina adzakuitanani kunyumba kwake ndipo nanunso mudzadya nsembe yakeyo.+

  • Levitiko 20:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 pamenepo ineyo ndidzam’kana munthu ameneyo pamodzi ndi banja lake,+ ndipo ndidzamupha pamodzi ndi onse ogwirizana naye pochita chiwerewere+ ndi Moleki, kuti asakhalenso pakati pa anthu awo.

  • Deuteronomo 31:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Iweyo ugona pamodzi ndi makolo ako,+ ndipo anthu awa adzaimirira+ ndi kuchita chiwerewere pakati pawo ndi milungu yachilendo ya m’dziko limene akupita.+ Iwo adzandisiya+ ndi kuphwanya pangano limene ndinapangana nawo.+

  • Yeremiya 3:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pali mawu akuti: “Mwamuna akathetsa ukwati ndi mkazi wake, ndipo mkaziyo n’kuchokadi ndi kukakwatiwa ndi mwamuna wina, sangabwererenso kwa mwamuna woyamba uja.”+

      Kodi dzikoli silinaipitsidwe kale?+

      Yehova wanena kuti: “Iwe wachita uhule ndi amuna ambirimbiri.+ Kodi m’poyenera kuti ubwererenso kwa ine?+

  • Ezekieli 23:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Iye sanasiye zauhule zake zimene anachokera nazo ku Iguputo. Aiguputowo anagona naye kuyambira ali kamtsikana. Iwo ndiwo anatsamira chifuwa chake ali namwali ndipo anali kuchita naye zachiwerewere.+

  • Yakobo 4:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Achigololo+ inu, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko n’kudziika pa udani ndi Mulungu?+ Choncho, aliyense amene akufuna kukhala bwenzi+ la dziko akudzisandutsa mdani wa Mulungu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena