Ekisodo 32:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Komabe Yehova anauza Mose kuti: “Amene wandichimwirayo ndi amene ndim’fafanize m’buku langa.+ Numeri 5:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 “‘Wansembeyo azilemba matemberero amenewa m’buku+ ndi kuwafafaniza+ m’madzi owawa aja. Deuteronomo 25:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Motero Yehova Mulungu wanu akakupumitsani kwa adani anu onse okuzungulirani, m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge kukhala cholowa chanu,+ mufafanize dzina la Amaleki pansi pa thambo.+ Musaiwale zimenezi. Deuteronomo 29:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Yehova sadzafuna kukhululukira+ munthu woteroyo, m’malomwake mkwiyo+ ndi ukali+ wa Yehova udzamuyakira,+ ndipo matemberero onse olembedwa m’buku+ ili adzakhala pa iye, motero Yehova adzafafanizadi dzina la munthuyo pansi pa thambo. Miyambo 10:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Anthu akamakumbukira zabwino zimene munthu wolungama anali kuchita, amam’dalitsa,+ koma dzina la anthu oipa lidzawola.+
19 Motero Yehova Mulungu wanu akakupumitsani kwa adani anu onse okuzungulirani, m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge kukhala cholowa chanu,+ mufafanize dzina la Amaleki pansi pa thambo.+ Musaiwale zimenezi.
20 Yehova sadzafuna kukhululukira+ munthu woteroyo, m’malomwake mkwiyo+ ndi ukali+ wa Yehova udzamuyakira,+ ndipo matemberero onse olembedwa m’buku+ ili adzakhala pa iye, motero Yehova adzafafanizadi dzina la munthuyo pansi pa thambo.
7 Anthu akamakumbukira zabwino zimene munthu wolungama anali kuchita, amam’dalitsa,+ koma dzina la anthu oipa lidzawola.+