7 Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha,+ wokhululukira zolakwa ndi machimo,+ koma wosalekerera konse wolakwa osam’langa.+ Wolanga ana, zidzukulu, ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo awo.”+
19 Ndiyeno Yoswa anauza anthuwo kuti: “Simungathe kutumikira Yehova, chifukwa iye ndi Mulungu woyera.+ Iye ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.+ Iye sadzakhululuka machimo anu ndi kupanduka kwanu.+