Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 28:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndikuika mwala mu Ziyoni+ kuti ukhale maziko. Umenewu ndi mwala+ wapakona woyesedwa,+ wamtengo wapatali,+ woti ukhale maziko olimba.+ Palibe munthu woukhulupirira amene adzade nkhawa.+

  • Zekariya 4:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Ngakhale pataikidwa chopinga chachikulu ngati phiri+ pamaso pa Zerubabele,+ chidzasalazidwa kukhala malo athyathyathya. Ndithu iye adzabweretsa mwala wotsiriza wa pakona.+ Akadzatero anthu adzafuula+ kuti: “Koma mwalawu ndiye ndi wokongola bwanji! Koma ndiye ndi wokongola!”’”+

  • Luka 20:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Koma iye anawayang’ana ndi kunena kuti: “Pajatu malemba amati, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana,+ umenewu wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.’+ Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani?

  • Machitidwe 4:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Yesu ameneyu ndiye ‘mwala umene inu omanga nyumba munauona ngati wopanda pake, umene tsopano wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.’+

  • 1 Akorinto 3:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Pakuti palibe munthu wina amene angayale maziko ena+ alionse kupatulapo amene anayalidwawo, omwe ndi Yesu Khristu.+

  • Aefeso 2:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Mwamangidwa pamaziko+ a atumwi+ ndi aneneri,+ ndipo Khristu Yesuyo ndiye mwala wapakona wa mazikowo.+

  • 1 Petulo 2:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Pakuti Lemba limati: “Inetu ndikuika mwala m’Ziyoni, mwala wochita kusankhidwa mwapadera, wapakona pa maziko, wamtengo wapatali, ndipo aliyense woukhulupirira sadzakhumudwa.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena