Genesis 6:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Tsopano nayi mbiri ya Nowa. Nowa anali munthu wolungama.+ Iye anali wopanda cholakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake. Nowa anayenda ndi Mulungu woona.+ Salimo 81:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Haa! Zikanakhala bwino ngati anthu anga akanandimvera,+Zikanakhala bwino ngati Isiraeli akanayenda m’njira zanga.+ Salimo 119:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 119 Odala ndi anthu osalakwitsa kanthu m’njira zawo,+Anthu amene akutsatira chilamulo cha Yehova.+ Mika 6:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Iwe munthu wochokera kufumbi, iye anakuuza zimene zili zabwino.+ Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo,+ ukhale wokoma mtima+ ndiponso uziyenda modzichepetsa+ ndi Mulungu wako.+ Luka 1:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Onse awiriwo anali olungama+ pamaso pa Mulungu chifukwa choyenda mokhulupirika,+ mogwirizana ndi malamulo onse+ komanso zofunika za m’chilamulo+ cha Yehova.+ Machitidwe 9:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Pamenepo mpingo+ mu Yudeya monse, mu Galileya, ndi mu Samariya unalowa m’nyengo yamtendere, ndipo unakhala wolimba. Popeza kuti unali kuyenda moopa Yehova+ ndiponso kulimbikitsidwa ndi mzimu woyera,+ mpingowo unali kukulirakulira. 1 Atesalonika 4:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Pomalizira abale, tinakulangizani za mmene muyenera kuyendera+ ndi mmene muyenera kukondweretsera Mulungu, ndipo mukuchitadi zimenezo. Tsopano tikufuna kukudandaulirani ndi kukupemphani m’dzina la Ambuye Yesu kuti mupitirize kuchita zimenezi mowonjezereka.+
9 Tsopano nayi mbiri ya Nowa. Nowa anali munthu wolungama.+ Iye anali wopanda cholakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake. Nowa anayenda ndi Mulungu woona.+
13 Haa! Zikanakhala bwino ngati anthu anga akanandimvera,+Zikanakhala bwino ngati Isiraeli akanayenda m’njira zanga.+
8 Iwe munthu wochokera kufumbi, iye anakuuza zimene zili zabwino.+ Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo,+ ukhale wokoma mtima+ ndiponso uziyenda modzichepetsa+ ndi Mulungu wako.+
6 Onse awiriwo anali olungama+ pamaso pa Mulungu chifukwa choyenda mokhulupirika,+ mogwirizana ndi malamulo onse+ komanso zofunika za m’chilamulo+ cha Yehova.+
31 Pamenepo mpingo+ mu Yudeya monse, mu Galileya, ndi mu Samariya unalowa m’nyengo yamtendere, ndipo unakhala wolimba. Popeza kuti unali kuyenda moopa Yehova+ ndiponso kulimbikitsidwa ndi mzimu woyera,+ mpingowo unali kukulirakulira.
4 Pomalizira abale, tinakulangizani za mmene muyenera kuyendera+ ndi mmene muyenera kukondweretsera Mulungu, ndipo mukuchitadi zimenezo. Tsopano tikufuna kukudandaulirani ndi kukupemphani m’dzina la Ambuye Yesu kuti mupitirize kuchita zimenezi mowonjezereka.+