Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 1:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Kenako Mulungu anati: “Tiyeni+ tipange munthu m’chifaniziro chathu,+ kuti akhale wofanana nafe.+ Ayang’anire nsomba zam’nyanja ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga, komanso nyama zoweta. Ayang’anirenso dziko lonse lapansi ndi nyama zonse zokwawa padziko lapansi.”+

  • Salimo 22:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Pakuti ndinu amene munanditulutsa m’mimba,+

      Amene munandichititsa kumva kuti ndine wotetezeka pamene ndinali kuyamwa mabere a mayi anga.+

  • Salimo 71:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga inu mwandithandiza.+

      Inu ndi amene munanditulutsa m’mimba mwa mayi anga.+

      Ndimatamanda inu nthawi zonse.+

  • Salimo 100:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu.+

      Iye ndi amene anatipanga, sitinadzipange tokha.+

      Ndife anthu ake ndi nkhosa zimene akuweta.+

  • Yesaya 44:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Yehova, amene anakupanga+ ndiponso amene anakuumba,+ amene anali kukuthandiza ngakhale pamene unali m’mimba,+ wanena kuti, ‘Usachite mantha,+ iwe mtumiki wanga Yakobo, ndiponso iwe Yesuruni,+ amene ndakusankha.

  • Yeremiya 1:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Ndisanakuumbe m’mimba,+ ndinakudziwa,+ ndipo usanatuluke m’mimbamo, ndinakusankha kuti uchite ntchito yopatulika.+ Ndinakusankha kuti ukhale mneneri ku mitundu ya anthu.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena