Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 11:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Choncho, tiyeni+ tipiteko kuti tikasokoneze+ chilankhulo chawo, kuti asamamvane polankhula.”+

  • Genesis 50:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Inu munali ndi cholinga chondichitira zoipa. Koma Mulungu anali ndi cholinga chabwino, kuti apulumutse miyoyo ya anthu ambiri ngati mmene akuchitira panomu.+

  • Yoswa 23:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 “Tsopano taonani! Ine ndatsala pang’ono kufa.+ Inu mukudziwa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe.+

  • Miyambo 21:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Palibe nzeru kapena kuzindikira kulikonse, kapena malangizo alionse otsutsana ndi Yehova.+

  • Danieli 4:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Iye amaona anthu onse okhala padziko lapansi ngati opanda pake+ ndipo amachita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake pakati pa makamu akumwamba ndi pakati pa anthu okhala padziko lapansi.+ Palibe aliyense amene angaletse dzanja+ lake kapena kumufunsa kuti, ‘Mukuchita chiyani?’+

  • Machitidwe 5:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 Koma ngati ikuchokera kwa Mulungu,+ simungathe kuwaletsa.+ Mukaumirira mukhoza kupezeka kuti mukulimbana ndi Mulungu.”+

  • Aheberi 6:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Mofanana ndi zimenezi, Mulungu pofuna kuwatsimikizira kwambiri anthu olandira lonjezolo monga cholowa chawo,+ kuti chifuniro chake n’chosasinthika,+ anachita kulumbira pa zimene analonjezazo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena