Salimo 45:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Zovala zako zonse ndi zonunkhira mafuta a mule, aloye ndi kasiya.*+Umasangalala ndi nyimbo zoimbidwa ndi zipangizo za zingwe, kuchokera m’chinyumba chachikulu cha mfumu, chokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu.+ Nyimbo ya Solomo 3:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 “Kodi chinthu chikuchokera kuchipululuchi n’chiyani, chooneka ngati utsi wokwera m’mwamba, chonunkhira mafuta a mule, lubani,*+ ndi mtundu uliwonse wa zonunkhira za ufa za munthu wamalonda?”+ Nyimbo ya Solomo 4:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Chikondi chimene umandisonyeza n’chokoma,+ iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga. Chikondi chimene umandisonyeza n’chabwino kuposa vinyo ndipo kununkhira kwa mafuta ako odzola n’koposa zonunkhira za mitundu yonse.+ Yohane 12:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Pamenepo Mariya anatenga mafuta onunkhira. Mafutawa anali nado+ weniweni, okwera mtengo kwambiri okwana magalamu 327. Mariya anathira mafutawo pamapazi a Yesu ndi kupukuta mapaziwo ndi tsitsi lake.+ M’nyumba monsemo munangoti guu kafungo kabwino ka mafutawo.
8 Zovala zako zonse ndi zonunkhira mafuta a mule, aloye ndi kasiya.*+Umasangalala ndi nyimbo zoimbidwa ndi zipangizo za zingwe, kuchokera m’chinyumba chachikulu cha mfumu, chokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu.+
6 “Kodi chinthu chikuchokera kuchipululuchi n’chiyani, chooneka ngati utsi wokwera m’mwamba, chonunkhira mafuta a mule, lubani,*+ ndi mtundu uliwonse wa zonunkhira za ufa za munthu wamalonda?”+
10 Chikondi chimene umandisonyeza n’chokoma,+ iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga. Chikondi chimene umandisonyeza n’chabwino kuposa vinyo ndipo kununkhira kwa mafuta ako odzola n’koposa zonunkhira za mitundu yonse.+
3 Pamenepo Mariya anatenga mafuta onunkhira. Mafutawa anali nado+ weniweni, okwera mtengo kwambiri okwana magalamu 327. Mariya anathira mafutawo pamapazi a Yesu ndi kupukuta mapaziwo ndi tsitsi lake.+ M’nyumba monsemo munangoti guu kafungo kabwino ka mafutawo.