2 Mafumu 9:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Kenako Yehu anafika ku Yezereeli,+ ndipo Yezebeli+ anamva zimenezo. Yezebeliyo anadzikongoletsa podzipaka utoto+ wakuda m’maso mwake n’kukongoletsanso tsitsi lake mochititsa kaso.+ Atatero anakaima pawindo n’kumayang’ana kunja.+ Esitere 1:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 kuti abweretse Mfumukazi Vasiti itavala duku lachifumu pamaso pa mfumu, kuti anthu onse ndi akalonga aone kuoneka bwino kwake, pakuti inalidi yokongola kwambiri.+ Miyambo 6:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Usasirire kukongola kwake mumtima mwako.+ Asakukope ndi maso ake owala,+ 1 Petulo 1:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Pakuti “anthu onse ali ngati udzu, ndipo ulemerero wawo wonse uli ngati duwa la udzu.+ Udzuwo umafota ndipo duwalo limathothoka,+
30 Kenako Yehu anafika ku Yezereeli,+ ndipo Yezebeli+ anamva zimenezo. Yezebeliyo anadzikongoletsa podzipaka utoto+ wakuda m’maso mwake n’kukongoletsanso tsitsi lake mochititsa kaso.+ Atatero anakaima pawindo n’kumayang’ana kunja.+
11 kuti abweretse Mfumukazi Vasiti itavala duku lachifumu pamaso pa mfumu, kuti anthu onse ndi akalonga aone kuoneka bwino kwake, pakuti inalidi yokongola kwambiri.+
24 Pakuti “anthu onse ali ngati udzu, ndipo ulemerero wawo wonse uli ngati duwa la udzu.+ Udzuwo umafota ndipo duwalo limathothoka,+