Nehemiya 2:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Ndiyeno mfumu inati: “N’chifukwa chiyani nkhope yako ili yachisoni+ pamene sukudwala? Pali chinachake chimene chikukuvutitsa mumtima.”+ Atanena zimenezi ndinachita mantha kwambiri. Salimo 38:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Ndasokonezeka ndipo ndawerama kwambiri chifukwa cha chisoni changa.+Ndayenda uku ndi uku tsiku lonse ndili wachisoni.+ Miyambo 15:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Mtima wachimwemwe umapangitsa nkhope kusangalala,+ koma chifukwa cha kupweteka kwa mtima munthu sasangalala.+ Mateyu 6:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 “Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuzani kuti: Lekani kudera nkhawa+ moyo wanu kuti mudzadya chiyani, kapena mudzamwa chiyani, kapenanso kuti mudzavala chiyani.+ Kodi moyo suposa chakudya, ndipo kodi thupi siliposa chovala?+
2 Ndiyeno mfumu inati: “N’chifukwa chiyani nkhope yako ili yachisoni+ pamene sukudwala? Pali chinachake chimene chikukuvutitsa mumtima.”+ Atanena zimenezi ndinachita mantha kwambiri.
6 Ndasokonezeka ndipo ndawerama kwambiri chifukwa cha chisoni changa.+Ndayenda uku ndi uku tsiku lonse ndili wachisoni.+
13 Mtima wachimwemwe umapangitsa nkhope kusangalala,+ koma chifukwa cha kupweteka kwa mtima munthu sasangalala.+
25 “Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuzani kuti: Lekani kudera nkhawa+ moyo wanu kuti mudzadya chiyani, kapena mudzamwa chiyani, kapenanso kuti mudzavala chiyani.+ Kodi moyo suposa chakudya, ndipo kodi thupi siliposa chovala?+