1 Samueli 22:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Pamapeto pake mfumu inauza Doegi+ kuti: “Iwe, tembenuka ukanthe ansembewa!” Nthawi yomweyo Doegi, Mwedomu,+ anatembenuka n’kukantha ndi kupha+ ansembewo tsiku limenelo, amuna 85 ovala efodi+ wa nsalu. 1 Mafumu 2:29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 29 Kenako Mfumu Solomo inauzidwa kuti: “Yowabu wathawira kuchihema cha Yehova, ndipo ali pambali pa guwa lansembe.” Choncho Solomo anatuma Benaya mwana wa Yehoyada, kuti: “Pita ukamuphe!”+ Miyambo 19:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu,+ koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pazomera.+ Miyambo 20:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Kuopsa kwa mfumu kuli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu.+ Aliyense woputa mkwiyo wake akuchimwira moyo wake womwe.+ Danieli 3:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Pamenepo Nebukadinezara anapsa mtima kwambiri+ ndipo analamula kuti abweretse Sadirake, Mesake ndi Abedinego.+ Choncho anabweretsadi amuna amphamvu amenewa pamaso pa mfumu.
18 Pamapeto pake mfumu inauza Doegi+ kuti: “Iwe, tembenuka ukanthe ansembewa!” Nthawi yomweyo Doegi, Mwedomu,+ anatembenuka n’kukantha ndi kupha+ ansembewo tsiku limenelo, amuna 85 ovala efodi+ wa nsalu.
29 Kenako Mfumu Solomo inauzidwa kuti: “Yowabu wathawira kuchihema cha Yehova, ndipo ali pambali pa guwa lansembe.” Choncho Solomo anatuma Benaya mwana wa Yehoyada, kuti: “Pita ukamuphe!”+
12 Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu,+ koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pazomera.+
2 Kuopsa kwa mfumu kuli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu.+ Aliyense woputa mkwiyo wake akuchimwira moyo wake womwe.+
13 Pamenepo Nebukadinezara anapsa mtima kwambiri+ ndipo analamula kuti abweretse Sadirake, Mesake ndi Abedinego.+ Choncho anabweretsadi amuna amphamvu amenewa pamaso pa mfumu.