5 Mwabwera kudzathandiza anthu amene akukondwera ndiponso amene akuchita zolungama,+ anthu amene amakukumbukirani potsatira njira zanu.+
Koma inuyo munakwiya+ chifukwa chakuti ifeyo tinkangopitirizabe kuchimwa+ kwanthawi yaitali. Choncho kodi ndife oyenera kupulumutsidwa?+