Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yobu 24:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Oipawo amakhala okwezeka kwa kanthawi, kenako n’kutha.+

      Iwo amatsitsidwa,+ ndipo mofanana ndi wina aliyense amathotholedwa.

      Amadulidwa mofanana ndi nsonga ya ngala za tirigu.

  • Mlaliki 6:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ndani angadziwe zabwino zimene munthu angachite pa moyo wake,+ masiku onse a moyo wake wachabechabe, umene umakhala ngati mthunzi?+ Pakuti ndani angamuuze munthu zimene zidzachitike padziko lapansi pano iyeyo atafa?+

  • Luka 12:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako adzaufuna.+ Nanga chuma chimene waunjikachi chidzakhala cha ndani?’+

  • Yakobo 1:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Dzuwa limatuluka ndi kutentha kwake n’kufotetsa zomera, ndipo maluwa a zomerazo amathothoka. Kukongola kwake kumatha. Momwemonso munthu wachuma adzafa akutsatira njira ya moyo wake.+

  • 2 Petulo 2:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Komanso chifukwa chosirira mwansanje, adzakudyerani masuku pamutu ndi mawu achinyengo.+ Koma chiweruzo chawo chimene chinagamulidwa kalekale+ chikubwera mofulumira, ndipo chiwonongeko chawo sichikuzengereza.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena