-
Mlaliki 9:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Zimene zimachitikira anthu onse n’zofanana.+ Pali mapeto amodzi+ kwa munthu wolungama+ ndi woipa,+ kwa munthu wabwino, woyera, ndi wodetsedwa, ndiponso kwa munthu amene amapereka nsembe ndi amene sapereka nsembe. Munthu wabwino n’chimodzimodzi ndi munthu wochimwa.+ Munthu amene amalumbira mosaganizira bwino n’chimodzimodzi ndi amene amaopa kulumbira.+
-
-
Mlaliki 9:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Nditaganizanso ndinaona kuti padziko lapansi pano anthu othamanga kwambiri sapambana pampikisano,+ amphamvu sapambana pankhondo,+ anzeru sapeza chakudya,+ omvetsa zinthu nawonso sapeza chuma,+ ndipo ngakhale odziwa zinthu sakondedwa,+ chifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.+
-