-
Yeremiya 26:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 “Mika+ wa ku Moreseti+ nayenso anali kunenera m’masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda.+ Iye anauza anthu onse a mu Yuda kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Ziyoni adzagawulidwa ngati munda,+ ndipo Yerusalemu adzangokhala milu ya mabwinja.+ Phiri la nyumba ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda za m’nkhalango.”’+
-
-
Ezekieli 36:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Tsopano inu mapiri a ku Isiraeli,+ tamverani mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, walankhula ndi mapiri, zitunda, mitsinje, zigwa ndi malo owonongedwa amene ndi mabwinja.+ Walankhulanso ndi mizinda yopanda anthu imene anthu otsala a mitundu ina anaitenga kukhala yawo. Anthuwo anakhala moizungulira ndipo amainyoza.+
-