-
Yesaya 9:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Ulamuliro wake wangati wa kalonga udzafika kutali+ ndipo mtendere sudzatha+ pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake, kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndi kukhala wolimba pogwiritsa ntchito chilungamo,+ ndiponso pogwiritsa ntchito mtima wowongoka,+ kuyambira panopa mpaka kalekale.* Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+
-
-
Yesaya 59:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Choncho iye anavala chilungamo monga chovala chodzitetezera chamamba achitsulo,+ ndiponso anavala chisoti cholimba chachipulumutso kumutu kwake.+ Kuwonjezera apo, anavala chilungamo monga chovala kuti akapereke chilango kwa adani ake+ ndiponso kuchita zinthu modzipereka kwambiri kunali ngati chovala chake chodula manja.+
-