Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 20:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Usaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,*+ wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.+

  • Ekisodo 34:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Pakuti simuyenera kugwadira mulungu wina,+ chifukwa Yehova, amene dzina lake ndi Nsanje, alidi Mulungu wansanje.*+

  • Deuteronomo 4:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi moto wowononga,+ iye ndi Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha basi.*+

  • Deuteronomo 6:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 (pakuti Yehova Mulungu wanu amene ali pakati panu ndi Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha basi).+ Musatsatire milungu ina kuopera kuti mkwiyo wa Yehova Mulungu wanu ungakuyakireni,+ ndipo angakufafanizeni padziko lapansi.+

  • Yoswa 24:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Ndiyeno Yoswa anauza anthuwo kuti: “Simungathe kutumikira Yehova, chifukwa iye ndi Mulungu woyera.+ Iye ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.+ Iye sadzakhululuka machimo anu ndi kupanduka kwanu.+

  • Yesaya 59:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Choncho iye anavala chilungamo monga chovala chodzitetezera chamamba achitsulo,+ ndiponso anavala chisoti cholimba chachipulumutso kumutu kwake.+ Kuwonjezera apo, anavala chilungamo monga chovala kuti akapereke chilango kwa adani ake+ ndiponso kuchita zinthu modzipereka kwambiri kunali ngati chovala chake chodula manja.+

  • Ezekieli 39:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Tsopano ndibweretsa ana a Yakobo omwe anatengedwa kupita kumayiko ena,+ ndipo ndichitira chifundo nyumba yonse ya Isiraeli.+ Nditeteza dzina langa loyera kuti lisadetsedwe.*+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena