Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake,+

      Ndipo adzamva chisoni chifukwa cha atumiki ake,+

      Chifukwa adzaona kuti thandizo lawachokera.

      Adzaona kuti pangokhala munthu wonyozeka ndi wopanda pake.

  • Salimo 103:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Monga mmene bambo amasonyezera chifundo kwa ana ake,+

      Yehova wasonyezanso chifundo kwa onse omuopa.+

  • Yesaya 60:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Alendo adzamanga mipanda yako,+ ndipo mafumu awo adzakutumikira.+ Ine ndinakulanga mu mkwiyo wanga,+ koma chifukwa cha kukoma mtima kwanga ndidzakuchitira chifundo.+

  • Maliro 3:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Chifukwa cha kukoma mtima kosatha+ kwa Yehova, ife sitinafafanizidwe,+ ndipo chifundo chake sichidzatha.+

  • Hoseya 11:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “Kodi ndikusiyirenji iwe Efuraimu?+ Kodi ndikuperekerenji kwa adani iwe Isiraeli?+ Kodi ndikusandutsirenji ngati Adima?+ Kodi ndikuchitirenji zofanana ndi zimene ndinachitira Zeboyimu?+ Mtima wanga wasintha+ ndipo pa nthawi imodzimodziyo wadzaza ndi chisoni.

  • Luka 15:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Choncho ananyamukadi n’kupita kwa bambo ake. Ali chapatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo anagwidwa chifundo. Pamenepo anamuthamangira ndi kumukumbatira ndipo anamupsompsona mwachikondi.

  • Yakobo 5:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Monga mmene mukudziwira, anthu amene anapirira timawatcha odala.+ Munamva za kupirira kwa Yobu+ ndipo mwaona zimene Yehova anamupatsa,+ mwaona kuti Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena