Ekisodo 11:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Ndipo atumiki anu onsewa adzatsika ndi kubwera kwa ine, n’kundigwadira ndi kundiweramira.+ Iwo adzanena kuti, ‘Pita, iweyo ndi anthu onse amene amakutsatira.’ Zitatero ndidzapitadi.” Atanena mawu amenewa anachoka kwa Farao atakwiya. Salimo 86:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Ikani chizindikiro cha ubwino wanu pa ine,Kuti anthu odana nane aone zimenezi ndi kuchita manyazi,+Pakuti inu Yehova mwandithandiza ndi kundilimbikitsa.+ Yesaya 45:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 kuti, ‘Zoonadi, kwa Yehova kuli chilungamo chonse ndi mphamvu.+ Onse omukwiyira adzabwereranso kwa iyeyo n’kuchita manyazi.+ Chivumbulutso 3:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Taona! Anthu ochokera m’sunagoge wa Satana, amene amanama+ kuti ndi Ayuda+ pamene si Ayuda, ndidzawachititsa kuti abwere kudzagwada ndi kuwerama+ pamapazi ako. Ndipo ndidzawachititsa kudziwa kuti ndimakukonda.
8 Ndipo atumiki anu onsewa adzatsika ndi kubwera kwa ine, n’kundigwadira ndi kundiweramira.+ Iwo adzanena kuti, ‘Pita, iweyo ndi anthu onse amene amakutsatira.’ Zitatero ndidzapitadi.” Atanena mawu amenewa anachoka kwa Farao atakwiya.
17 Ikani chizindikiro cha ubwino wanu pa ine,Kuti anthu odana nane aone zimenezi ndi kuchita manyazi,+Pakuti inu Yehova mwandithandiza ndi kundilimbikitsa.+
24 kuti, ‘Zoonadi, kwa Yehova kuli chilungamo chonse ndi mphamvu.+ Onse omukwiyira adzabwereranso kwa iyeyo n’kuchita manyazi.+
9 Taona! Anthu ochokera m’sunagoge wa Satana, amene amanama+ kuti ndi Ayuda+ pamene si Ayuda, ndidzawachititsa kuti abwere kudzagwada ndi kuwerama+ pamapazi ako. Ndipo ndidzawachititsa kudziwa kuti ndimakukonda.