16 Anthu akhungu ndidzawayendetsa m’njira imene sakuidziwa.+ Ndidzawadutsitsa mumsewu umene sakuudziwa.+ Malo amdima ndidzawasandutsa kuwala pamaso pawo,+ ndipo malo okumbikakumbika ndidzawasalaza.+ Zimenezi ndi zimene ndidzawachitire ndipo sindidzawasiya.”+