Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 43:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “Ine ndanena ndipo ndapulumutsa.+ Pa nthawi imene pakati panu panalibe mulungu wachilendo,+ ine ndinachititsa kuti chipulumutsocho chimveke. Choncho inuyo ndinu mboni zanga,+ ndipo ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.+

  • Yesaya 44:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Anthu inu musachite mantha ndipo musathedwe nzeru.+ Kodi sindinachititse aliyense wa inu kuti amve kuyambira nthawi imeneyo? Kodi sindinakuuzeni zimenezi?+ Inu ndinu mboni zanga.+ Kodi palinso Mulungu kupatulapo ine?+ Ayi, palibe Thanthwe.+ Sindikudziwapo aliyense.’”

  • Yohane 15:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 ndipo inunso mudzachitira umboni,+ chifukwa mwakhala nane kuchokera pa chiyambi.

  • Machitidwe 1:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Koma mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu.+ Pamenepo mudzakhala mboni+ zanga mu Yerusalemu,+ ku Yudeya konse ndi ku Samariya,+ mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”+

  • 1 Akorinto 15:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Ndiponso, ndiye kuti ifenso takhala mboni zonama za Mulungu,+ chifukwa tachita umboni+ wonamizira Mulungu kuti anaukitsa Khristu+ pamene sanamuukitse, ngati akufa sadzaukadi.+

  • Chivumbulutso 1:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Komanso, kuchokera kwa Yesu Khristu, “Mboni Yokhulupirika,”+ “Woyamba kubadwa kuchokera kwa akufa,”+ ndiponso “Wolamulira wa mafumu a dziko lapansi.”+

      Kwa iye amene amatikonda,+ amenenso anatimasula ku machimo athu ndi magazi ake enieniwo,+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena