Yesaya 36:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Kodi milungu ya Hamati+ ndi Aripadi+ ili kuti? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu?+ Kodi yalanditsa Samariya m’manja mwanga?+ Yesaya 37:38 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 38 Pamene Senakeribu anali kugwada m’kachisi wa mulungu wake+ Nisiroki,+ ana ake Adarameleki ndi Sarezere anamupha ndi lupanga,+ iwo n’kuthawira kudziko la Ararati.+ Kenako Esari-hadoni+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake. Yesaya 45:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 “Sonkhanani pamodzi n’kubwera kwa ine.+ Unjikanani pamodzi, inu anthu opulumuka ku mitundu ya anthu.+ Amene amanyamula chifaniziro chawo chosema chamtengo sadziwa kanthu, mofanana ndi amene amapemphera kwa mulungu woti sangawapulumutse.+ Yesaya 46:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Iwo amamunyamula pamapewa awo.+ Amamutenga n’kukamuika pamalo ake ndi kumuimika bwinobwino. Mulunguyo sayenda kuchoka pamalo akewo.+ Ngakhale munthu atamufuulira, iye sayankha. Sapulumutsa munthu kumavuto ake.+
19 Kodi milungu ya Hamati+ ndi Aripadi+ ili kuti? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu?+ Kodi yalanditsa Samariya m’manja mwanga?+
38 Pamene Senakeribu anali kugwada m’kachisi wa mulungu wake+ Nisiroki,+ ana ake Adarameleki ndi Sarezere anamupha ndi lupanga,+ iwo n’kuthawira kudziko la Ararati.+ Kenako Esari-hadoni+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.
20 “Sonkhanani pamodzi n’kubwera kwa ine.+ Unjikanani pamodzi, inu anthu opulumuka ku mitundu ya anthu.+ Amene amanyamula chifaniziro chawo chosema chamtengo sadziwa kanthu, mofanana ndi amene amapemphera kwa mulungu woti sangawapulumutse.+
7 Iwo amamunyamula pamapewa awo.+ Amamutenga n’kukamuika pamalo ake ndi kumuimika bwinobwino. Mulunguyo sayenda kuchoka pamalo akewo.+ Ngakhale munthu atamufuulira, iye sayankha. Sapulumutsa munthu kumavuto ake.+