-
1 Mafumu 18:26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Choncho anatenga ng’ombe yaing’ono yamphongo imene Eliya anawapatsa, n’kuikonza. Kenako anayamba kuitana dzina la Baala kuyambira m’mawa mpaka masana. Ankaitana kuti: “Inu a Baala, tiyankheni!” Koma sipanamveke mawu alionse,+ ndipo palibe anayankha.+ Iwo anapitiriza kudumphadumpha ngati akuvina, kuzungulira guwa lansembe limene anamanga.
-
-
Yona 1:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Zitatero oyendetsa chombo anayamba kuchita mantha ndipo aliyense anayamba kufuulira mulungu wake+ kuti amuthandize. Iwo anayamba kuponya m’nyanja katundu amene anali m’chombomo kuti chipepukidwe.+ Apa n’kuti Yona atatsikira mkatikati mwa chombocho, pakuti chinali ndi zipinda zapansi. Kumeneko Yona anagona tulo tofa nato.+
-