Yeremiya 50:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Pakuti mtundu wina wabwera kudzamuukira kuchokera kumpoto.+ Umenewu ndi mtundu umene wasandutsa dziko lake kukhala chinthu chodabwitsa, moti m’dzikoli mulibe aliyense wokhalamo.+ Anthu ndiponso ziweto zathawa.+ Zonse zapita.”+ Yeremiya 51:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 “Nolani mivi yanu.+ Dzitetezeni ndi zishango zozungulira, amuna inu. Yehova wautsa mitima ya mafumu a Amedi,+ chifukwa akufuna kulanga Babulo ndi kumuwononga.+ Yehova akufuna kubwezera Babulo chilango chifukwa cha kachisi wake.+ Danieli 5:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 “PERESI,* ufumu wanu wagawanika ndipo waperekedwa kwa Amedi ndi Aperisiya.”+
3 Pakuti mtundu wina wabwera kudzamuukira kuchokera kumpoto.+ Umenewu ndi mtundu umene wasandutsa dziko lake kukhala chinthu chodabwitsa, moti m’dzikoli mulibe aliyense wokhalamo.+ Anthu ndiponso ziweto zathawa.+ Zonse zapita.”+
11 “Nolani mivi yanu.+ Dzitetezeni ndi zishango zozungulira, amuna inu. Yehova wautsa mitima ya mafumu a Amedi,+ chifukwa akufuna kulanga Babulo ndi kumuwononga.+ Yehova akufuna kubwezera Babulo chilango chifukwa cha kachisi wake.+