4 popeza mwanayo asanadziwe kuitana+ kuti, ‘Ababa!’ kapena ‘Amama!’ anthu adzanyamula chuma cha ku Damasiko ndi katundu wolandidwa ku Samariya n’kupita naye pamaso pa mfumu ya Asuri.”+
“Awa ndi mawu a Yehova oweruza dziko la Hadiraki, ndipo akuweruzanso Damasiko.+ Pakuti maso a Yehova akuyang’ana anthu+ komanso mafuko onse a Isiraeli.