2 Yosiya anachita zoyenera pamaso pa Yehova+ ndipo anayenda m’njira zonse za Davide kholo lake.+ Iye sanapatukire mbali ya kudzanja lamanja kapena lamanzere.+
25 Panalibenso mfumu ina iye asanakhale mfumu imene inabwerera+ kwa Yehova ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse,+ ndi mphamvu zake zonse, mogwirizana ndi chilamulo chonse cha Mose. Ngakhale pambuyo pake sipanakhalenso mfumu ina ngati iyeyo.