Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 1:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Musamakondere poweruza.+ Munthu wamba ndi munthu wolemekezeka onse muziwamvetsera chimodzimodzi.+ Musamaope munthu+ chifukwa mukuweruzira Mulungu.+ Mlandu umene wakuvutani muziubweretsa kwa ine kuti ndiumve.’+

  • 2 Samueli 8:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Davide anapitiriza kulamulira Isiraeli+ yense ndipo nthawi zonse anali kupereka zigamulo ndi kuchita chilungamo+ kwa anthu ake onse.+

  • Salimo 58:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndipo mtundu wa anthu udzati:+ “Ndithudi wolungama adzalandira mphoto.+

      Ndithudi pali Mulungu amene akuweruza dziko lapansi.”+

  • Salimo 72:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Aweruzire anthu milandu mwachilungamo,+

      Ndipo aweruze milandu ya osautsika ndi ziweruzo zolungama.+

  • Yesaya 11:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka+ ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa a padziko lapansi. Adzakwapula dziko lapansi ndi ndodo ya pakamwa pake,+ ndipo adzagwiritsa ntchito mzimu wa pakamwa pake kupha munthu woipa.+

  • Yeremiya 22:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Yehova wanena kuti: “Muzichita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo, muzilanditsa munthu amene anthu achinyengo akufuna kumulanda katundu wake. Musachitire nkhanza mlendo aliyense wokhala m’dziko lanu, mwana wamasiye* kapena mkazi wamasiye.+ Musawachitire zachiwawa.+ Musakhetse magazi a munthu aliyense wosalakwa m’dziko lino.+

  • Yohane 7:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Lekani kuweruza poona maonekedwe akunja, koma muziweruza ndi chiweruzo cholungama.”+

  • Aheberi 1:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Unakonda chilungamo ndipo unadana ndi kusamvera malamulo. N’chifukwa chake Mulungu, Mulungu wako, anakudzoza+ ndi mafuta achikondwerero chachikulu kuposa cha mafumu ena.”+

  • Chivumbulutso 19:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndipo nditayang’ana ndinaona kumwamba kutatseguka, kenako ndinaona hatchi yoyera.+ Wokwerapo wake dzina lake linali Wokhulupirika+ ndi Woona.+ Iyeyo anali kuweruza ndi kumenya nkhondo mwachilungamo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena