4Tamverani mawu a Yehova inu ana a Isiraeli. Yehova ali ndi mlandu ndi anthu okhala m’dzikoli,+ chifukwa m’dzikoli mulibe choonadi,+ kukoma mtima kosatha, ndiponso anthu a m’dzikoli amachita zinthu ngati kuti sadziwa Mulungu.+
2 Inu mapiri, imvani mlandu umene Yehova ali nawo pa anthu ake. Inu matanthwe okhazikika, tamverani. Mvetserani inu maziko a dziko lapansi,+ pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi anthu ake. Iye azenga mlandu Aisiraeli, kuti:+