7 Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anamangira Kemosi+ malo okwezeka,+ chinthu chonyansa+ cha Mowabu, paphiri+ lomwe linali patsogolo+ pa Yerusalemu. Anamangiranso Moleki malo okwezeka, yemwe ndi chinthu chonyansa cha ana a Amoni.
13 Malo okwezeka amene anali kutsogolo+ kwa Yerusalemu kudzanja lamanja* la Phiri Lachiwonongeko,* amene Solomo+ mfumu ya Isiraeli inamangira Asitoreti+ chonyansa cha Asidoni, Kemosi+ chonyansa cha Mowabu, ndi Milikomu+ chonyansa cha ana a Amoni, mfumuyo inawasandutsa osayenera kulambirako.