Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Iwe usanafike, ndidzachititsa anthuwo mantha*+ ndipo Ahivi, Akanani ndi Ahiti adzathawiratu pamaso pako.+

  • Ekisodo 34:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Koma inu sungani zimene ndikukulamulani lero.+ Inetu ndikuthamangitsa pamaso panu Aamori, Akanani, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+

  • Numeri 33:53
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 53 Mukalande dzikolo n’kukhalamo, chifukwa ndidzalipereka ndithu kwa inu kuti likhale lanu.+

  • Deuteronomo 7:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Muwononge anthu a mitundu yonse amene Yehova Mulungu wanu akuwapereka kwa inu.+ Musawamvere chisoni+ ndipo musatumikire milungu yawo+ chifukwa kuchita zimenezo kudzakutcherani msampha.+

  • Deuteronomo 9:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Sikuti mukulowa m’dziko ili kukalitenga kukhala lanu chifukwa cha kulungama kwanu+ kapena chifukwa cha kuwongoka mtima kwanu.+ Yehova Mulungu wanu akukankhira mitundu iyi kutali ndi inu, kwenikweni chifukwa cha kuipa kwawo,+ ndiponso kuti Yehova akwaniritse mawu onse amene analumbirira makolo anu Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo.+

  • Deuteronomo 18:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Pakuti aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova. Ndipo chifukwa chakuti anthu a mitundu ina akuchita zimenezi, Yehova Mulungu wako akuwapitikitsa pamaso pako.+

  • 2 Mbiri 20:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Kodi inuyo Mulungu wathu+ si paja munathamangitsa anthu amene anali kukhala m’dziko lino pamaso pa anthu anu Aisiraeli,+ n’kulipereka+ kwa mbewu ya Abulahamu yemwe anali kukukondani,+ kuti likhale lawo mpaka kalekale?

  • Salimo 44:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Munapitikitsa anthu a mitundu ina ndi dzanja lanu,+

      Ndipo m’malo mwawo munakhazikitsa anthu anu.+

      Munagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuipitikitsa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena