Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 23:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Mulungu si munthu, woti anganene mabodza,+

      Si mwana wa munthu, woti angadzimve kuti ali ndi mlandu.+

      Kodi ananenapo kanthu koma osachita,

      Analankhulapo kanthu kodi koma osakwaniritsa?+

  • 2 Mafumu 23:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Komabe Yehova sanabweze mkwiyo wake waukulu umene unayakira Yuda,+ chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene Manase anawachititsa, n’kukwiyitsa nazo Mulungu.+

  • Yesaya 43:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 “Komanso, nthawi zonse ine sindisintha.+ Palibenso wina amene angathe kupulumutsa anthu m’dzanja langa.+ Ndikayamba kuchitapo kanthu,+ ndani amene angalimbane ndi dzanja langa?”+

  • Yesaya 46:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambira pa chiyambi.+ Kuyambira kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinachitike.+ Ine ndiye amene ndimanena kuti, ‘Zolingalira zanga zidzachitikadi,+ ndipo ndidzachita chilichonse chimene ndikufuna.’+

  • Ezekieli 24:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Tsoka lako lidzabwera ndithu+ ndipo ndidzachitapo kanthu. Sindidzazengereza,+ kumva chisoni+ kapena kusintha maganizo.+ Iwo adzakuweruza mogwirizana ndi njira zako ndi zochita zako.+ Ine Yehova ndanena,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena