Numeri 24:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Iye ataona Akeni,+ anapitirizanso mawu ake a ndakatulo, kuti:“Mokhala mwanu ndi mokhazikika, malo okhala inu ali pathanthwe. Salimo 55:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Ndipo ndikunena kuti: “Ndikanakhala ndi mapiko ngati njiwa!+Ndikanauluka ndi kukakhala kwina.+ Nyimbo ya Solomo 2:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Iwe njiwa yanga,+ tuluka m’malo obisika a pathanthwe. Tuluka pamalo osaoneka m’mphepete mwa njira yotsetsereka. Ndikufuna ndione thupi lako lokongola.+ Ndikufuna kumva mawu ako, chifukwa mawu ako ndi okoma ndipo iweyo ndiwe wokongola.’”+ Yeremiya 49:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Iwe unachititsa anthu kunjenjemera ndiponso unali ndi mtima wodzikuza,+ koma zimenezi zakunyenga, iwe amene ukukhala m’malo obisika a m’thanthwe pamwamba pa phiri. Ngakhale kuti umamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga+ ndidzakugwetsa kuchoka pamenepo,”+ watero Yehova.
21 Iye ataona Akeni,+ anapitirizanso mawu ake a ndakatulo, kuti:“Mokhala mwanu ndi mokhazikika, malo okhala inu ali pathanthwe.
14 Iwe njiwa yanga,+ tuluka m’malo obisika a pathanthwe. Tuluka pamalo osaoneka m’mphepete mwa njira yotsetsereka. Ndikufuna ndione thupi lako lokongola.+ Ndikufuna kumva mawu ako, chifukwa mawu ako ndi okoma ndipo iweyo ndiwe wokongola.’”+
16 Iwe unachititsa anthu kunjenjemera ndiponso unali ndi mtima wodzikuza,+ koma zimenezi zakunyenga, iwe amene ukukhala m’malo obisika a m’thanthwe pamwamba pa phiri. Ngakhale kuti umamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga+ ndidzakugwetsa kuchoka pamenepo,”+ watero Yehova.