6 Ife tamva za kunyada kwa Mowabu, kuti ndi wonyada kwambiri.+ Tamva za kudzikweza kwake, kunyada kwake, ndi mkwiyo wake.+ Zolankhula zake zodzitukumula sizidzachitika.+
10 Anthu amenewo adzaona zimenezi chifukwa cha kunyada kwawo,+ komanso chifukwa chakuti anali kunyoza ndi kudzikweza pamaso pa anthu a Yehova wa makamu.+