29 “Tamva za kunyada kwa Mowabu.+ Iye ndi wodzikuza kwambiri. Tamva za kudzikweza kwake, kunyada kwake, kudzikuza kwake ndi kudzitukumula kwa mtima wake.”+
10 Anthu amenewo adzaona zimenezi chifukwa cha kunyada kwawo,+ komanso chifukwa chakuti anali kunyoza ndi kudzikweza pamaso pa anthu a Yehova wa makamu.+