11 Ndinaonanso akuluakulu 70+ a nyumba ya Isiraeli ataimirira. Yaazaniya mwana wa Safani+ anali ataima pakati pawo. Iwo anaima pamaso pa zojambulazo, aliyense atanyamula chiwaya chofukizira nsembe m’manja mwake. Utsi wonunkhira wa zofukizazo unali kukwera m’mwamba.+