19 Tsopano tumizani uthenga ndipo musonkhanitse Aisiraeli onse kwa ine paphiri la Karimeli.+ Musonkhanitsenso aneneri 450 a Baala+ ndi aneneri 400 a mzati wopatulika,+ amene amadya patebulo la Yezebeli.”+
16 Anasiya malamulo onse+ a Yehova Mulungu wawo n’kudzipangira zifaniziro ziwiri za ana a ng’ombe,+ zopangidwa ndi zitsulo zosungunula,+ komanso mzati wopatulika.+ Anayamba kugwadira khamu lonse la zinthu zakuthambo+ ndi kutumikira Baala.+