Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Oweruza 3:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Chotero ana a Isiraeli anachita zoipa pamaso pa Yehova, ndipo anaiwala Yehova Mulungu wawo,+ moti anayamba kutumikira Abaala+ ndi mizati yopatulika.+

  • Oweruza 10:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Zitatero, ana a Isiraeli anayambanso kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndipo anayamba kutumikira Abaala,+ zifaniziro za Asitoreti,+ milungu ya ku Siriya,+ milungu ya ku Sidoni,+ milungu ya ku Mowabu,+ milungu ya ana a Amoni+ ndi milungu ya Afilisiti.+ Motero iwo anasiya Yehova ndipo sanam’tumikire.+

  • 1 Samueli 7:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Zitatero, Samueli anauza nyumba yonse ya Isiraeli kuti: “Ngati mukubwereradi kwa Yehova+ ndi mtima wanu wonse, chotsani milungu yachilendo pakati panu.+ Muchotsenso zifaniziro za Asitoreti,+ ndi kulunjikitsa mitima yanu kwa Yehova mosayang’ananso kwina,+ ndi kutumikira iye yekha. Mukatero, adzakupulumutsani m’manja mwa Afilisiti.”+

  • 1 Mafumu 11:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Solomo anayamba kutsatira Asitoreti,+ mulungu wamkazi wa Asidoni, ndi Milikomu,+ chonyansa cha Aamoni.

  • 2 Mafumu 23:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Malo okwezeka amene anali kutsogolo+ kwa Yerusalemu kudzanja lamanja* la Phiri Lachiwonongeko,* amene Solomo+ mfumu ya Isiraeli inamangira Asitoreti+ chonyansa cha Asidoni, Kemosi+ chonyansa cha Mowabu, ndi Milikomu+ chonyansa cha ana a Amoni, mfumuyo inawasandutsa osayenera kulambirako.

  • Salimo 106:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Anayamba kutumikira mafano awo,+

      Ndipo mafanowo anakhala msampha wawo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena