31 “Munthu mmodzi wothamanga wakumana ndi mnzake, ndipo mthenga mmodzi wakumana ndi mnzake,+ onsewa akukanena kwa mfumu ya Babulo kuti mzinda wake walandidwa kumbali zonse.+
8 Ndiye chifukwa chake m’tsiku limodzi, miliri yake idzafika. Miliri yakeyo+ ndiyo imfa, kulira, ndi njala. Ndipo adzanyekeratu ndi moto+ chifukwa Yehova Mulungu, amene anamuweruza, ndi wamphamvu.+