Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 29:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Pamenepo anthu adzanena kuti, ‘N’chifukwa chakuti anataya pangano+ la Yehova Mulungu wa makolo awo, limene anapangana nawo pamene anali kuwatulutsa m’dziko la Iguputo.+

  • 1 Mafumu 9:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Ndipo adzati, ‘N’chifukwa chakuti anasiya Yehova Mulungu wawo amene anatulutsa makolo awo m’dziko la Iguputo.+ M’malomwake, anatenga milungu ina+ n’kumaigwadira ndi kuitumikira. N’chifukwa chake Yehova anawabweretsera tsoka lonseli.’”+

  • Yeremiya 2:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 “Koma iwe ukuti, ‘Ine ndilibe mlandu uliwonse. Ndithudi mkwiyo wake wandichokera.’+

      “Tsopano ndikuyamba kukuimba mlandu chifukwa chonena kuti, ‘Sindinachimwe.’+

  • Yeremiya 13:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Ukadzanena mumtima mwako kuti,+ ‘N’chifukwa chiyani zinthu zimenezi zandigwera?’+ pamenepo udzadziwe kuti wavulidwa siketi yako+ ndipo zidendene zako zazunzidwa chifukwa zolakwa zako zachuluka.

  • Yeremiya 16:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “Ndiyeno ukadzauza anthu awa mawu onsewa, ndipo iwo akadzakufunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova wanena kuti adzatigwetsera tsoka lalikulu limeneli? Kodi talakwa chiyani ndipo tamuchimwira chiyani Yehova Mulungu wathu?’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena