14 iyenso* adzakupatsani mvula pa nthawi yake m’dziko lanu,+ mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza,+ ndipo mudzakololadi mbewu zanu ndi kukhaladi ndi vinyo wotsekemera* komanso mafuta.
23 Inu ana aamuna a Ziyoni kondwerani ndi kusangalala chifukwa cha Yehova Mulungu wanu.+ Iye adzakupatsani mvula yoyambirira pa mlingo woyenera+ ndipo adzakugwetserani mvula yamvumbi, mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza, ngati mmene zinalili poyamba.+