Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 28:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Yehova ndiye mphamvu yanga+ ndi chishango changa.+

      Mtima wanga umam’khulupirira.+

      Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukukondwera.+

      Ndidzamutamanda mwa kumuimbira nyimbo yanga.+

  • Yesaya 12:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “Fuula mwachisangalalo iwe mkazi wokhala mu Ziyoni, pakuti Woyera wa Isiraeli ndi wamkulu pakati pako.”+

  • Yesaya 41:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Udzapeta+ mapiri ndi zitundazo ndipo mphepo idzaziuluza.+ Mphepo yamkuntho idzaziuluzira kumalo osiyanasiyana.+ Iweyo udzasangalala chifukwa cha Yehova.+ Udzadzitama chifukwa cha Woyera wa Isiraeli.”+

  • Yesaya 61:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndithu ine ndidzakondwera mwa Yehova.+ Moyo wanga udzasangalala ndi Mulungu wanga.+ Pakuti iye wandiveka zovala zachipulumutso.+ Wandiveka malaya akunja achilungamo odula manja,+ ngati mkwati amene wavala chovala chakumutu mofanana ndi wansembe,+ ndiponso ngati mkwatibwi amene wavala zinthu zake zodzikongoletsera.+

  • Habakuku 3:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Ine ndidzakondwerabe mwa Yehova+ ndipo ndidzasangalala mwa Mulungu wachipulumutso changa.+

  • Zekariya 10:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 A nyumba ya Efuraimu adzakhala ngati munthu wamphamvu+ ndipo adzasangalala mumtima mwawo ngati kuti amwa vinyo.+ Ana awo aamuna adzaona zimenezi ndipo adzakondwera.+ Mitima yawo idzakondwera chifukwa cha Yehova.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena