Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 26:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 ndidzakugwetserani mvula pa nthawi yake.+ Nthaka idzakupatsani chakudya,+ ndipo mitengo ya m’munda idzakupatsani zipatso zake.+

  • Deuteronomo 28:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Yehova adzakutsegulira kumwamba, nyumba yake yabwino yosungiramo zinthu, kuti akupatse mvula pa nyengo yake+ m’dziko lako ndi kuti adalitse ntchito iliyonse ya manja ako.+ Udzakongoza mitundu yambiri koma iwe sudzakongola kanthu kwa iwo.+

  • Salimo 65:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Mizere yawo imakhathamira, ndipo zibuma zake zimasalazidwa,+

      Ndipo mumafewetsa nthaka ndi mvula yamvumbi. Mumadalitsa zomera m’nthakayo.+

  • Yesaya 30:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Mulungu adzabweretsa mvula pambewu zanu zimene munabzala munthaka,+ ndipo zokolola za munthakayo zidzakhala chakudya chopatsa thanzi.+ M’tsiku limenelo, ziweto zanu zidzadya msipu pamalo aakulu odyetserapo ziweto.+

  • Yeremiya 14:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Kodi pakati pa mafano opanda pake a mitundu ya anthu pali fano lililonse+ limene lingagwetse mvula? Kapena kodi kumwamba pakokha kungagwetse mvula yamvumbi?+ Kodi si inu Yehova Mulungu wathu+ amene mumachititsa zimenezi? Chiyembekezo chathu chili mwa inu chifukwa ndinu amene mumachititsa zonsezi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena