Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Yehova adzakutsegulira kumwamba, nyumba yake yabwino yosungiramo zinthu, kuti akupatse mvula pa nyengo yake+ m’dziko lako ndi kuti adalitse ntchito iliyonse ya manja ako.+ Udzakongoza mitundu yambiri koma iwe sudzakongola kanthu kwa iwo.+

  • Salimo 135:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Amachititsa nthunzi kukwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+

      Iye anapanganso zipata zotulukirapo mvula.+

      Amachititsa mphepo kutuluka m’nkhokwe zake.+

  • Salimo 147:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Muimbireni Iye amene amaphimba mapiri ndi mitambo,+

      Amene amakonza mvula kuti igwe padziko lapansi,+

      Amenenso amameretsa udzu wobiriwira m’mapiri.+

  • Yesaya 30:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Mulungu adzabweretsa mvula pambewu zanu zimene munabzala munthaka,+ ndipo zokolola za munthakayo zidzakhala chakudya chopatsa thanzi.+ M’tsiku limenelo, ziweto zanu zidzadya msipu pamalo aakulu odyetserapo ziweto.+

  • Yoweli 2:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Inu ana aamuna a Ziyoni kondwerani ndi kusangalala chifukwa cha Yehova Mulungu wanu.+ Iye adzakupatsani mvula yoyambirira pa mlingo woyenera+ ndipo adzakugwetserani mvula yamvumbi, mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza, ngati mmene zinalili poyamba.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena