Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 14:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Tsopano Mose anatambasula dzanja lake kuloza panyanja,+ ndipo Yehova anachititsa mphepo yamphamvu yakum’mawa kuyamba kugawa nyanjayo usiku wonse ndi kuumitsa pansi pake.+ Motero madziwo anali kugawikana.+

  • Numeri 11:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Kenako Yehova anautsa mphepo+ yamkokomo kuchokera kunyanja. Mphepoyo inabweretsa zinziri,+ ndipo inazimwaza kuyambira pamsasapo mpaka pamtunda woyenda tsiku limodzi kulowera mbali ina, ndiponso mtunda woyenda tsiku limodzi kulowera mbali inayo. Inazimwaza kuzungulira msasawo, moti zinali kuuluka m’munsi kwambiri pafupifupi mikono* iwiri kuchokera pansi.

  • Salimo 78:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Anachititsa mphepo ya kum’mawa kuwomba m’mlengalenga,+

      Ndipo mwa mphamvu zake anachititsa mphepo ya kum’mwera kuwomba.+

  • Salimo 107:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Aona mmene amautsira mphepo yamkuntho mwa kungonena mawu,+

      Moti nyanjayo imachita mafunde.+

  • Salimo 147:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Amatumiza mawu ake+ ndi kusungunula madzi oundanawo.

      Amachititsa mphepo yake kuwomba,+

      Ndipo madzi amayenda.

  • Yona 1:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndiyeno Yehova anabweretsa chimphepo champhamvu panyanjapo,+ ndipo panachita mkuntho wamphamvu.+ Chotero chombocho chinatsala pang’ono kusweka.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena