Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide.
65 Inu Mulungu, anthu akukutamandani mu Ziyoni+ ndipo akhala chete pamaso panu,
Iwo adzakwaniritsa malonjezo awo kwa inu.+
2 Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu.+
4 Wodala ndi munthu amene inu mwamusankha ndi kumuyandikizitsa kwa inu,+
Kuti akhale m’mabwalo anu.+
Tidzakhutira ndi zinthu zabwino za m’nyumba yanu,+
Malo anu oyera kapena kuti kachisi wanu woyera.+
5 Mudzatiyankha ndi zinthu zochititsa mantha zochitika mwachilungamo,+
Inu Mulungu wa chipulumutso chathu,+
Inu Chidaliro cha malire onse a dziko lapansi ndi anthu okhala pafupi ndi nyanja zakutali.+
7 Iye akutontholetsa phokoso la nyanja,+
Akutontholetsa phokoso la mafunde ake komanso chipwirikiti cha mitundu ya anthu.+
8 Ndipo anthu okhala m’madera akutali adzachita mantha ndi zizindikiro zanu,+
Mudzachititsa kulowa ndi kutuluka kwa dzuwa kufuula mokondwera.+
9 Inu mwatembenukira dziko lapansi kuti mulipatse zinthu zochuluka,+
Mwalilemeretsa kwambiri.
Mtsinje wochokera kwa Mulungu ndi wosefukira ndi madzi.+
Munalinganiza zinthu, kuti mbewu zawo zibale.+
Umu ndi mmene mumaperekera zinthu padziko lapansi.+
10 Mizere yawo imakhathamira, ndipo zibuma zake zimasalazidwa,+
Ndipo mumafewetsa nthaka ndi mvula yamvumbi. Mumadalitsa zomera m’nthakayo.+