Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 51:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Mundisambitse bwinobwino ndi kuchotsa cholakwa changa,+

      Ndiyeretseni ku tchimo langa.+

  • Salimo 78:38
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 Koma anawamvera chifundo.+ Anali kukhululukira* machimo awo+ ndipo sanali kuwawononga.+

      Nthawi zambiri anali kubweza mkwiyo wake,+

      Ndipo sanali kuwasonyeza ukali wake wonse.

  • Salimo 79:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Tithandizeni inu Mulungu wa chipulumutso chathu,+

      Kuti dzina lanu lilemekezedwe.+

      Tipulumutseni ndi kutikhululukira* machimo athu chifukwa cha dzina lanu.+

  • Yesaya 1:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Yehova akuti, “Bwerani tsopano anthu inu. Tiyeni tikambirane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine.+ Ngakhale machimo anu atakhala ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.+ Ngakhale atakhala ofiira ngati magazi, adzayera ngati thonje.

  • Yohane 1:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Tsiku lotsatira anaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo anati: “Taonani, Mwanawankhosa+ wa Mulungu amene akuchotsa uchimo+ wa dziko!+

  • Aheberi 9:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 kuli bwanji magazi+ a Khristu, amene anadzipereka wopanda chilema kwa Mulungu kudzera mwa mzimu wamuyaya?+ Kodi magazi amenewo sadzayeretsa+ zikumbumtima zathu ku ntchito zakufa,+ kuti tichite utumiki wopatulika+ kwa Mulungu wamoyo?

  • 1 Yohane 1:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Komatu, ngati tikuyenda m’kuunika ngati mmene iye alili m’kuunika,+ ndiye kuti ndife ogwirizana,+ ndipo magazi+ a Yesu Mwana wake akutiyeretsa+ ku uchimo wonse.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena