23 Inu ana aamuna a Ziyoni kondwerani ndi kusangalala chifukwa cha Yehova Mulungu wanu.+ Iye adzakupatsani mvula yoyambirira pa mlingo woyenera+ ndipo adzakugwetserani mvula yamvumbi, mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza, ngati mmene zinalili poyamba.+